Angozo James Matemba amachokera Kwa Bvumbwe ku Thyolo koma wakulila Ku Blantyre Chigumula m’mudzi otchedwa Chiwaya.
Anabadwila ku Mulambala m’mudzi mwa amfumu Agunde chipatala cha Anambado mu chaka cha 1986 ndipo ali ndi zaka 37.Bambo ake kwao ndi kuchiri kumulambala komweko.
Kuimba adayamba mu chaka cha 2011 kulowa mu studio momwe adajambula nyimbo yake yoyamba yomwenso idali mutu wa album yake yoyamba Bwela kwa Yesu ku Studio ya Samuel Muula yotchedwa SM Records. Then adayamba kujambula nyimbo zina yekha ku JM Records then adayamba kugwila ntchito ndi W Music Entertainment, Bizo Beats Komanso Hands Eye Beats by Peter Komanso Seleti Records. Album yake yachiwiri adatulutsa mu 2018. wajambula album ya nambala 3 yomwe watulutsa ndipo adayipanga launch pa 3 December 2023.