Ndi gulu loyimba nyimbo za Uzimu lomwe limapezeka ku Lilongwe,Mitundu m’mudzi mwa Kambanizithe .Gululi linayamba pa 1 December 2021,m’mbuyomu Choir ya Ana inalipo koma ndikalekale kwambiri.
Yemwe anayambitsa Choir yi pa 1 December 2021 ndi Weston Godfrey ndipo anayambitsa ali ndi zaka 19 zakubadwa. Ngakhale Choir yi inayamba koma panalibe podalira makamaka pa nkhani ya za chuma ndipo izi zidachititsa a Weston kuti apeke nyimbo yopempha thandizo yomwe anatumiza kwa anthu osiyanasiya, nyimboyi inapangitsa Thawale Nursery Choir kupeza yunifolomu komanso ndalama zojambulira chimbale komanso kupanga launch chimbale chomvera komanso chowonera choyamba chomwe mutu wake ndi “Ponda Buleki” chomwe chinatuluka pa 7 May 2023.Kungobwererako m’mbuyo pang’ono Weston anatsogolerapo Choir ya Kasupe Nursery yomwe ndi prayer House ya Thawale.