Lucy Chipembere anabadwa ndi kukulira m’boma la Kasungu koma kwawo kwa makolo ake ndi ku Dowa ndi Dedza kwa mai ndi bambo mu mndandanda otero.Ndipo iye anabadwa pa 15 July 1994 m’banja la ana anayi,iye ndi wachitatu kubadwa.
Dzina lake lenileni ndi Lucy Mtenje,ndipo la Chipembere ndi la mwamuna wake, amene nthawi zambiri ndi yemwe amapeka ndi kulemba nyimbo ndipo awiriwa adapanga gulu lotchedwa “Khalani Tcheru enter.”Dzina la LadyGenius adamupatsa ndi mwamuna wake kuti lifanane ndi lake lodyera la “Grandgenius”.
Lucy adalowa mu studio koyamba mu chaka cha 2019, ndipo luso lake lidafika podziwika bwino mu 2020 atayimba nyimbo yake ya chiwiri “Mundigwire dzanja”, imene idafika poseweredwa mu mawailesi station odziwika monga Mbc komanso Times.
Iye ali ndi ana awiri, wa mkazi ndi wamamuna ndipo maina awo ndi Harris aka PAPAGENIUS komanso Hazel aka QueenGenius.