Juliet Kunje Kazipeze anabadwira ku Bangwe mu mzinda wa Blantyre pa 10 March 1987, koma kumudzi kwawo ndi kwa Chitera ku Chiladzuru,ndipo m’banja mwawo anabadwa ana 4 iye ndi wa number 3 ndipo wakulira ku Bangwe ku Blantyre.
Music yake anayamba ali wang’ono anali wa praise team ku school group la Scom ndipo mu 2019 Juliet anajambula nyimbo yake yoyamba yotchedwa mwayenera ndipo kuonjezera pa kuimba Juliet ndi evangelist mayitanidwe ake ochokera kumwamba.
Juliet waphunzira school yake pa Namatapa Primary ku Bangwe komanso ku Nankhaka Primay School ku Lilongwe area 30, Secondary School yake waphunzira pa Chinamwali Private Secondary School ku Zomba.Atalemba mayeso Juliet anapanga course ya Hotel and Management ku college ina ( I P D ) Ku Mtonya mu mzinda wa Blantyre , wagwirapo ntchito ku Blantyre Lodge.
Juliet anakwatiwa ndi Mr Willie Kazipeze omwe ndi manager akenso mu music yake ndipo ali ndi ana 4.