King William Chirwa Contacts:0996091516/0885606368
King William Chirwa Anabadwila ku Kasungu, Mtunthama trading center, T.A Wimbe. Anabadwa pa 18 January 1993 mu banja la ana 7 , anyamata 5 , atsikana 2. Ndipo king William Chirwa ndi second born.
Atabadwa Anapatsidwa dzina loti Ganizani , ndipo atakula anasintha yekha kukhala William. Adasintha dzina chifukwa dzina la Ganizani mudali Milandu ya Kumudzi.
King William Chirwa adakwatila 2018 pa 1 September anakwatila ku ntchisi mkazi wake ndi Flyness Banda ndipo pano ali ndi ana awili: daughter Malanatha Chirwa and boy Mordecai Chirwa.
Adayamba kuimba ali mwana akuti amkathawa mu class kumakaimba ku mabwalo la zamasewela. Akachoka ku school amzake pomwe akupita kokasewela mpila iye amapita kumakaimba zitini zakutha ndikumapanga nyimbo mpaka adayamba kumunena kuti ndi osokosela.
Kulowa ku studio adayamba 2016 koma vuto lidali la za chuma nyimbo zimangothela mu phone mwake.Atapeza ndalama adapita ku studio yodziwika bwino mu Lilongwe C.L Touch komwe producer wake ndi Viwe Chibwana komwe adaimba nyimbo ya ( Ona, Ona, Ona, Mbuye Yesu ndiye Yankho) nyimbo iyi ndiyo idayamba kumuika pa Map anayamba kudabwa kuti Gulu la wanthu likukonda nyimboyi.
Tsiku Lina munthu wina adamuitana ndikupeleka ndalama kuti akaimbenso nyimbo ina koma adamuuza kuti ndimene wayimbila nyimbo ya Yankho kuyambila pomwepo iye adzintchedwa King William Chirwa ndipo umu ndim’mene dzina loti King William Chirwa lidayambila.
Pano King William Chirwa ali ndi nyimbo zokoma kwambiri zokwana 4 nyimbozi anthu amalephela kusankhapo yabwino kwambiri chifukwa zonse ndi nyimbo zokoma kwambiri.
Kupatula kuimba King William Chirwa ndi M’busa amatumikila Mpingo wa Malawi Assemblies of God ndipo pano akutumikila ku Lilongwe.
Analemba mayeso a Form 4 , 2013 ndi 2014 ndipo pano ali ndi Diploma in Theology.
Pano King William Chirwa akudziwika ndi nyimbo izi : Yankho, Walipila, Hossanah, komamso Kulitsani Malile anga ndipo nyimbo imodzi producer ndi Viwe Chibwana wa ku C.L Touch Studio, zitatu producer ndi DJ Lobodo ndipo King William Chirwa ali ndi plan yopanga promotion nyimbo zake kuyambila January 2024.
King William Chirwa Contacts:0996091516/0885606368