Oyimba wina wa nyimbo za uzimu m’dziko muno yemwe amakhala ku Johannesburg m’dziko la South Africa Litah Lubano Nine watulutsa nyimbo yatsopano yotchedwa ndavomera lero.
Nyimbo ya ndavomera yomwe ndiyabwino komanso yotsitsimutsa ikukamba za kuvomera mayitanidwe a Mulungu. Nyimboyi yajambulidwa mwapamwamba komanso mwaukatswiri kwambiri ku Slate Music Records ndi Alex Chilambula ndipo ikupezeka pa malawigospelmusic.com.
Pomufunsa Litah za mawu ake otsiriza iye adalimbikitsa anthu omwe akumutumikira Mulungu kuti asatope kamba koti pakadali pano anthu atangwanika ndi zinthu zam’dziko.