Chorus
Tizasonkhana tonse
Patsiku loweruza
Pomwe zintchito
Zathu zatichitira
Umboni
Tipemphere kwakuya
Tikagwa mayesero
Tingazaphonyane
Nacho chipulumutso
Verse 1
Tikamakhala padziko
Tisamayiwalire
Kuti tsiku lina tizaweruzidwaso
Aliyense azadza pamaso
Patate kuzalandira mphoto monga
Zintchito zake
Tiyeni tikonzeke
Tilape machimo
Tsiku lakudza mbuye
Kulibe kulapaaaaaa
Monga m’busa achitira
Oweta ziweto khosa
Kumanja mbuzi
Kumanzere
Chorus
Zasonkhana tonse
Patsiku loweruza
Pomwe zintchito
Zathu zachitira umboni
Tipemphere kwakuya
Nkagwa mayesero
Tingazaphonyane
Nacho chipulumutso
Verse 2
Kwayikika kwamunthu
Azafa kamodzi ndipo
Atafa adikilira mphoto
Lapiratu m’balewe
Udakali ndimoyo
Tsiku lobwera mbuye
Kulibe kulapa
Kulibe kulapa kulibe kulapa kulibe kulapa
Kulibe kulapa
Chorus
Zasonkhana tonse
Patsiku lomaliza
Pomwe zintchito zathu
Zachitira umboni
Tipemphere kwakuya
Tikagwa mayesero
Tingazaphonyane
Nacho chipulumutso
Verse 3
Likalira lipenga lotsirizalo onse
Oyera mtima
Azakwatulidwa
Komwe kulibe
Nthenda njala
Kulibe tizangoyimba
Kutitu tagonjetsa
Lapiratu m’balewe
Ukadali ndimoyo
Chimwemwe chosantha
Mwamba chikudikira iwe
Chorus
Tizasonkhana tonse
Tizasonkhana tonse
Tsiku loweruza pomwe zintchito zanthu zachitira umboni
Tipemphere
Tipemphere kwakuya
Nkagwa mayesero
Tingazaphonyane
Nacho chipulumutso ×2