M’dziko lathu lino la Malawi tili ndi oyimba nyimbo za uzimu ochuluka komanso osiyanasiyana aluso omwe amayimba zamba zosiyanasiyana mwapamwamba komanso modabwitsa. koma sitingakambe za oyimbawa osatchulapo dzina la oyimba wina waluso Grecium Nyambo.
Mukakhala pansi ndikupanga kauniuni wanu mudzapeza kuti Grecium Nyambo ndim’modzi mwa oyimba amene amayimba Raggae yabwino kwambiri m’dziko muno.
Polankhulana ndi a Nyambo za chifukwa chomwe iwo adasankha kumayimba nyimbo zawo m’chamba cha raggae chokhachokha iwo adati “Ndikaimba raggae anthu amayamikira komanso uthenga umaperekedwa bwino”.Komabe ngakhale izi zili chomwechi a Nyambo anayimbanso nyimbo zina zomwe zili m’zamba zina monga Osova Mavuto yomwe ili m’chamba cha Amapiano komanso raggae, Mulikonze yomwe inayimbidwa m’chamba cha Afro yosakanikira yonkela ku mbira.
Ndikaimba raggae anthu amayamikira komanso uthenga umaperekedwa bwino
Nyambo
Grecium adayamba kuyimba m’chaka cha 2003 koma m’mene chimafika chaka 2018 katswiriyu adayamba kuyimba nyimbo za uzimu. Chisomo komanso chita chokomela Mulungu ndi nyimbo zina mwa izo zomwe adatulutsa m’chaka cha 2018. Nyambo Sadatulutse chimbale pakadali pano koma nyimbo zomwe alinazo zapazokha mzopitilira khumi.pomufunsa chifukwa chimene adayambira kuyimba nyimbo za uzimu Nyambo adati: “Moyo wanga ndadutsa muzambiri ndipo ndamuona Mulungu akundimenyera nkhondo komanso ndi chida chimene ndimadalira Ndiye ndikuyenera kulalikira komanso kuchitira umboni za ubwino wake adatero a Nyambo poyankha kwawo”.
Moyo wanga ndadutsa muzambiri ndipo ndamuona Mulungu akundimenyera nkhondo komanso ndi chida chimene ndimadalira Ndiye ndikuyenera kulalikira komanso kuchitira umboni za ubwino wake
Nyambo yemwe akusonkhanitsa nyimbo zake zonse m’chachachi kuti atulutse chimbale chake wati akufuna awapatsire a Malawi mayimbidwe a Live ndi Band yake yomwe adayambitsa yotchedwa Stars Vibration.
Nyambo ndi mwana wachinayi kubadwa m’banja la ana Asanu ndi atatu ndipo amagwira ntchito kuwailesi komanso Kanema wa Timveni ngati broadcasting engineer ndipo amakhala ku Area 25 mumzinda wa Lilongwe.
Article by Harris Msosa
2 comments
One of the best gospel musicians in Malawi,,, proud of you brother, keep the fire burning
One of the best gospel musicians in Malawi,,, proud of you brother, keep the fire burning