Mary Mhone anabadwa mu chaka cha 1988 ndipo m’banja mwawo anabadwa ana asanu ndipo iye ndi wachinayi kubadwa ndipo amakhala ku Pretoria dera lotchedwa Haertbeatsport Dam Schoemans Vill m’dziko la South Africa,kumudzi kwawo ndi ku Nkhatabay Chisala koma pano anakhazikika ku Mzuzu.
![](https://www.malawigospelmusic.com/wp-content/uploads/2024/04/IMG-20240423-WA0004.jpg)
Mary anayamba kuyimba mu chaka cha 2020 koma chimbale choyamba anatulutsa mu 2022 chotchedwa Alipo Yesu ndipo pakadali pano ali mkati mojambula chimbale chake chachiwiri.