Chimwemwe Mandala amachokera m’mudzi mwa Samuti T/A Chimaliro m’boma la Thyolo ndipo anabadwa m’chaka cha 1987.
Chimwemwe anayamba kuyimba kale kwambiri ali mwana koma mbuyo monsemu zimakhala zovutirapo kwa iye kupitiliza mayimbidwe ake kamba kavuto la za chuma kotero mu chaka cha 2019 ndipamene anayambanso kuyimba pomwe anatulutsa chimbale chake chotchedwa By My Side chomwe anajambula ndi DJ Lobodo m’dziko la South Africa.
Pakadali pano Chimwemwe akujambula chimbale chake chachiwiri chotchedwa Ndapepukidwa komanso akujambula chimbale chanyimbo zowonela cha “By My Side” zomwe akuganiza kuzikhazikitsa zonse pakamodzi.
Chimwemwe akukhalira m’dziko la South Africa komwe akukhala ndi mkazi wake komanso mwana wake.