Gelson Mahala anabadwa pa 14 may 1999 ku chipatala cha Malamulo T/A Khwethemule, Thyolo ndipo pano amakhalira m’mudzi mwa Jekete mfumu yayikulu Mpama boma la Chiradzulu.
![](https://www.malawigospelmusic.com/wp-content/uploads/2024/04/IMG-20240413-WA0001-683x1024.jpg)
M’banja lawo anabadwamo ana 7, akazi awiri,amuna asanu ndipo iye ndi wa number 4 kubadwa.Gelson anayamba kuyimba pa 28 November 2018.
Chiyambi chake chakuyimba chinali chovutilapo ndithu chifukwa Kuntundu wakwawo kulibeko munthu oyimba komanso ngakhale anabadwira kubanja lachikhristu makwaya sankayimba nawo.
“Nditabadwa mwatsopano 2016 ndinayamba kumva mayitanidwe otumikira Mulungu ndipo ndimakakamizika kwambiri Kutumikira Mulungu kudzera mukuyimba ndipo ndimkamva bwino kwambiri ndikamamvera nyimbo makamaka pa radio program ija ya Gospel Top 20 ndipo ndikapeza munthu akuyimba nyimbo ankandisangalasa kwambiri” anatero Gelson.”Ndinayamba kupeka nyimbo zosiyanasiyana ndipo ndinkawapatsa athu kuti aziyimba komanso ndinkaziphuzitsa ku kwaya ya mpingo wathu”adawonjezera kulankhula moteromo Gelson.
![](https://www.malawigospelmusic.com/wp-content/uploads/2024/04/IMG-20240413-WA0003-683x1024.jpg)
Nyimbo zonse zimene wayimba Gelson zilipo 12 ndipo anazitolera ndikuziyika pamodzi ngati chimbale chotchedwa Ndinu Mulungu ndipo pakatipa watulutsapo nyimbo imodzi yotchedwa Ndaliwona Dzanja Lanu komanso pali nyimbo ina imene sinatuluke yotchedwa Ndi Ineyo komanso Uzichepetse imene wayimba mothandizana ndi Favour Chimpini ndipo zonsezi zituluka pa 20 mwezi omwe uno.