Patrick Simon Kangere anabadwa pa 11 May 1979 ndipo anayamba kuyimba mu chaka cha 1999. Mubanja mwawo anabadwa ana 9 atsikana atatu, anyamata 6 ndipo iwo ndi wa number 4.
Pakadali pano Pastor Simon akukhalira ku Durban m’dziko la South Africa koma ku Malawi kobadwira ndi ku Mulanje kwa Chinakanaka koma komwe amakhala ndi Ndirande mumzinda wa Blantyre.
Frank Mmemoh anabadwa pa 24 February 1980 ndipo anayamba kuyimba cha m’ma 2000.
M’banja mwawo anabadwamo ana 7 amuna anayi akazi atatu koma imfa inatengapo awiri adatsala ana asanu amuna atatu akazi awiri ndipo iye ndiwa number 5 kubadwa ndipo pakadali pano akukhala m’dziko la South Africa ndipo amagwira ntchito pa company ina ngati dalayivala.
Pastor Simon amayimba limodzi ndi mzawo Frank Mmemoh ndipo pakadali pano atulutsa nyimbo zina zatsopano zomwe ali ndi chikonzero choti adzazikhazikitse chimbale chawo chotchedwa Bvomera mu June chaka cha mawa.