Rabson Mchizi anabadwa pa 18 December 1995, pa Ekwendeni hospital m’boma la Mzimba ndipo anabadwa mu nyumba ya ana 5 amuna 4 Mkazi m’modzi ndipo ndi mwana oyamba amene wakulila moyenda kwambili chifukwa Cha ntchito ya bambo ake.
Kuyimba anayamba pakanthawi ndipo wakhala akuyimbitsa choir ya Emanyaleni Children Dance Choir.Muchaka cha 2017 ndipamene anadzatulutsa chimbale chawo choyamba title Mayankho m’menemo muli nyimbo 11 ,kuchoka pamenepo anadzaona kuti Mulungu anali naye ntchito ndipamene anayamba kuganiza zotulusa nyimbo zake payekha ndipo zinachitika mu chaka cha 2023 ndipamene anatulutsa chimbale chake chotchedwa ‘Bwezi Lenileni’ chimene chinajambulidwa ndi CYM Studio ndipo chinakhazikitsidwa mothandizidwa ndi Evance Meleka,Gift Monile komanso Mathews Ziyabwanya.
Ulendo wake wakhala ovuta koma chikhulupililo chilipo kuti akafika chifukwa iye si okwatira ndipo ali mu mpingo wa Faith Ministries Church ndipo amangopanga za business.